Bakili Muluzi Tv @bakilimuluzitv Channel on Telegram

Bakili Muluzi Tv

@bakilimuluzitv


Official Telegram Of Bakili Muluzi Tv 📺

Bakili Muluzi Tv (English)

Are you a fan of Bakili Muluzi and want to stay updated on all things related to him? Look no further than Bakili Muluzi Tv! This official Telegram channel is dedicated to bringing you the latest news, updates, and exclusive content about Bakili Muluzi. Whether you're interested in his political career, personal life, or achievements, this channel has got you covered. Join us today to be a part of the Bakili Muluzi community and never miss out on any important information. Don't wait, subscribe now to Bakili Muluzi Tv and be the first to know everything about this iconic figure!

Bakili Muluzi Tv

21 Feb, 16:53


Zelensiky wazungulira mutu ngati zipani za Tonse alliance

Bakili Muluzi Tv

21 Feb, 05:49


Tibwerezenso lero paja amati mphini yobwereza kuwala.

Ngati umasapota chipani ndie ukufuna kumva zokomera chipani chakocho, pita ku ma page a zipani.
Bakili Muluzi tv simayimira chipani chilichonse; timakamba nkhani imene ilipo.

Pamene timakamba za imfa ya Chilima palibe ku UTM amene anatigula. Masapota a UTM musamatiuze chochita ngati kuti page ndi ya UTM. Osatipanga force kuti tizinyoza Chakwera chifukwa udani wanuwo sukutikhudza. Ife timadzudzula Chakwera mogwirizana ndi mavuto a za chuma & not politics. I hope tamvana.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

19 Feb, 16:44


Nyanja ya m'baibulo yayamba kuphwera modabwitsa

Bakili Muluzi Tv

16 Feb, 19:33


SONA

Bakili Muluzi Tv

15 Feb, 19:27


Ukalamba ophatikiza ndi matenda; HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

14 Feb, 16:55


Mulungu wabalalitsa mizimu 9 ya Satana Mdyerekedzi

Bakili Muluzi Tv

13 Feb, 19:24


2025 tikhala tikulimbana ndi atsogoleri onse oyendera mphepo. Dziko la Malawi laonongeka chifukwa cha zipani za anthu abodza.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

13 Feb, 18:44


A UTM mukhoza kupita kumene mungamve zokusangalatsani. Auzeni anyamata anu amene akunyoza APM akuuzeni za imfa ya Chilima komanso azinyoza boma. Monse mwayambira kunyinyirika pano vuto lanu ndi chani? Munabwera nokha and you are free to go wherever you like. Ife ngati Bakili Muluzi tv munatipeza mudzatisiyanso chimodzimodzi.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

13 Feb, 18:18


Kufatsa si kupusa; Taonani a Kabambe apepera

Bakili Muluzi Tv

11 Feb, 19:26


Opposition simachita fund page ya Bakili Muluzi tv. Zikuoneka kuti ambiri mumasangalala tikanyoza ena koma tikabwera pa inu mukukwiya. Ife si ma campaign director a opposition ndipo simunatilembe ntchito yonyoza anthu. Timachita mwakufuna kwathu & not by force.

Kupanga adverise pa Page yathu ndi njira imodzi yopezera ndalama kuti tipitilize kupanga ma video.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

11 Feb, 16:55


Kodi muli ndi zochitika? Mukufuna uthenga wanu umveke pa Bakili Muluzi tv?

Advertising tiyamba posachedwa. Kaya ndi misonkhano ya zipani za ndale; UDF, AFFORD, DPP, PP, MCP, UTM, PDP; Aliyense ngolandilidwa pa Page pano.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

11 Feb, 16:39


A science apeza msnkhwala a edzi a pamwamba. Anthu asiye kumwa ma ARV; Kwabwera Jamison wa mphamvu.

Bakili Muluzi Tv

10 Feb, 16:35


Ma billion amene amatolera mdzina la chipani,anatenga ndi a kubanja. No wonder chipani chinayikidwa pa Sale after his death. Akanapanga bwanji ndalama za chipani anatenga ndi a kubanja.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

10 Feb, 12:29


Mlendo olemekezeka ku mwambo okhazikitsa SKC foundation, ndi president Dr Lazarus Chakwera komanso Madam Her Excellency Monica Chakwera.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

10 Feb, 12:04


Akufuna tizinyoza Chakwera koma akudana nazo tikamanyoza Chilima. Ndie uchitsiruwo.

Mesa onsewa anali limodzi zaka 4?
We don't work by emotions like UTM blind followers.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

10 Feb, 08:56


Zadziwika tsopano kuti asilikali oposa 600 a dziko la Rwanda anaphedwa pamene M23 imalanda mzinda wa Goma. Achibale anali odabwa kuona boma la Paul Kagame likuwabweletsera mitembo. Ngakhale mwambo wa maliro umakhala wa changu komanso amaletsa kuona nkhope.

Asilikali atatu a Malawi, 14 South Africa komanso mmodzi Uruguay, anaphedwa ku DRC. President Dr Lazarus Chakwera walamula Army commander, ayambiretu process yosamutsa asilikali athu ku DRC.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

10 Feb, 06:29


"Malamulo a chipani chimodzi takana. Ndi chifukwa chani kukula kwa a Mutharika, akumva kuwawa ndi a MCP?

Hon Peter Mukhito, DPP Secretary General

Bakili Muluzi Tv

09 Feb, 18:27


MCP mogwirizana ndi makhothi, akufuna kulepheletsa Mutharika asayime pa Chisankho.

Bakili Muluzi Tv

09 Feb, 09:17


Kupatula imfa ya Israella Bushiri komanso kuzunza Norman Chisale, Steven Kayuni anatseka bank account ya Peter Mutharika kuyambira 2020 up-to-date.

M'bale wake Kezzie Msukwa atalandira Benz ndi 20 million kwa Sattar, anamuteteza kuti asamangidwe. Anatsogoleranso kumangidwa kwa former ACB director, Martha Chizuma. Mkulu wakale wa police George Kainja, atalandira Truck kwa Sattar, iyeyu anamuteteza kuti asamangidwe.

Mr Steven Kayuni ndi amene anasainira kuti Gerald Viola amangidwe pankhani zosamveka. Akuti anapereka LPO kwa munthu kuti achite supply chimanga ku NFRA chikhalirecho NFRA simagula chimanga pogwiritsa ntchito LPO. Anapanga ma document a bodza pofuna kumupereka. Komabe a khothi adapeza kuti ndi nkhani yopepera ndipo anapereka suspended sentence kwa Mr Gerald Viola. Steven Kayuni sanasangalale ndi chigamulo cha khothi ndipo anachita appeal mpaka Viola anakaseva ndende kwa zaka ziwiri.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

09 Feb, 00:15


"Tikamanena mfundo tidziunikiranso dziko lino kuti zoipa zimene akupanga anthu ena tizidziwa.
Tikamapanga zisankho tipange zisankho zabwino.
Ndie mmbuyomu ndimanena munatukwana; ulendo uno ndikufuna mukatukwane zenizeni.

Kumunena munthu kuti ngwakuba ataba, sikumunyozayi koma nkunena zoona. Anthu akuba tatopa nawo; anthu abodzanso tatopa nawo!! Kaya mutuma anthu adzitisaka, tiyeni dzitisakani. Enanso muli pompano akutumani, imvani zenizeni mukanene."

Mawu a Dr Saulos Chilima mu 2020

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

08 Feb, 19:14


Prophet Bushiri wamudandaula Steven Kayuni, mnzake wa Kamajekete.

Bakili Muluzi Tv

07 Feb, 14:55


UTM ili ngati plan ya America ku Gaza

Bakili Muluzi Tv

06 Feb, 21:25


Akuluakulu! History is the best teacher.

Palibe angafute olo kamba atadikula.

Bakili Muluzi Tv

06 Feb, 19:15


Ndi munthu wa misala yekha amene angayerekeze Kabambe ndi Mutharika. Dziko lonse linaona Blantyre ili pa Full Holiday chifukwa cha APM.
You cannot compare a Lion with a mere barking dog.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

06 Feb, 14:10


Trump wayimitsa chithandizo chifukwa cha kuchuluka kwa katangale.

USAID was a Criminal Organisation.

Bakili Muluzi Tv

06 Feb, 05:55


Mavuto a za chuma sakutanthauza kuti opposition yogawanikana komanso yodzikonda ingagwetse Chakwera.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

06 Feb, 05:05


Ngati zipani, muli ndi ma Page amene mumachita fund. Bakili Muluzi tv simapangidwa fund ndi chipani.Timang'alura pamene taona ndipo sitipembedza mafano osema.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

05 Feb, 15:13


A UTM asiye kupanga blame Dr Lazarus Chakwera ndi Prof Peter Mutharika pa mavuto opanga okha.

Bakili Muluzi Tv

05 Feb, 08:04


Mwini wake Chilima anavomereza ndi pakamwa pake kuti amayendetsa nawo dziko lino. Inu ndi ndani kuti mukatsutse zimenezi?

UTM kunachuluka blind followers. 2018 amachita blame Prof Peter Mutharika; Leronso akulimbana ndi Dr Lazarus Chakwera nkumamuyeretsa Chilima as if he was an angel.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

04 Feb, 14:52


Wakufa sadziwika; Chinsinsi cha imfa chili ndi mwini Namalenga

Bakili Muluzi Tv

04 Feb, 07:17


Breaking News!

Paul Kagame walamula asilikali ake kuti achoke ku DRC mwansanga. Izi zachitika pomwe South Africa ikutumiza zida zoopsa komanso asilikali ku DRC. Rwanda yachita mantha itaona zimenezi ndipo akuganiza kuti Ramaphosa akukonzekera nkhondo yoopsa ndi Kagame.

Tikupatsirani zambiri zikamachitika.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

04 Feb, 06:39


Amene mukukayika kuti sine Bakili Muluzi tv, mudikire lero nding'alure pang'ono nkhani ya Chilima. I think ndi zomwe mukufuna kuti ndichite kuyiyankhulira mwa nthawi zonse. Mwina kulemba kokhaku sikukukwanira.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

04 Feb, 04:31


Akuti Bakili Muluzi TV samakamba za munthu wakufa. Nthawi yomwe timanena za Kamuzu ndi John Tembo nkuti muli kuti? Mbiri zonse za achina Idi Amin zija ndi anthu amoyo? Audio ya 1992 tinayika ija inali ya anthu a moyo?

In fact former president Bakili Muluzi atalonjeza nsapato, anthu amamukumbutsabe mpaka lero, ndie sikuti tingasiye kukumbutsa malonjezo a 2020 ngakhale kuti olonjezayo kulibe.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

03 Feb, 20:12


Good night Malawi

Bakili Muluzi Tv

03 Feb, 19:26


Mwina enanu mukutitsatira kumene.

Ifetu poyamba Dr Chakwera timawayamikira akachita zabwino. Ngakhale misonkhano yawo timaponya pa YouTube. Koma tinasiya Kamajekete atayamba mwano. A UTM musatitole chifukwa timakufufuzirani imfa ya Chilima. Ife timadana ndi mwano.

Bakili Muluzi Tv

03 Feb, 19:18


Mupite ku YouTube channel chathu mukaone mmene timanyozera Chilima ali ndi moyo since 2020. Ife si a UTM & will never be.

Bakili Muluzi Tv

03 Feb, 19:13


Aliyense olemba ma comment opusa ndizingochita ban asa comentenso.

Bakili Muluzi Tv

03 Feb, 19:11


Kodi anyamata a UTM mukulira chani pa page pano? Kapena munatilemba ganyu yonyoza boma la Chakwera komanso kukamba imfa ya Chilima?

Monse mwayambira kuti page yahackidwa, yahackidwayo ndi page ya amanu? Kapena amene tinakuuzani kuti mupange mgwirizano mu 2020 tinali ife?
Ifetu sitinakhalepo ndi chipani, timang'alura pamene taona.

Bakili Muluzi Tv

03 Feb, 17:38


Chifukwa cha nkhondo ku DRC, Rwanda ikhoza kuluza contract yake ndi matimu a PSG komanso Arsenal (VISIT RWANDA).

Pali nkhawa yakuti ndalama za Kagame ndi za magazi a anthu amene akuphedwa ku DRC chifukwa cholimbirana miyala ya mtengo wa patali. Potero matimuwa sangakhalenso ndi chidwi chosapota dziko la mwazi.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

03 Feb, 17:06


1. Dzulo president wa Burundi waopseza Kagame.
2. Dzana M23 yayamba operation yofuna kulanda mzinda wa Bukavu.
3. Dzulo former Rwandan General, Kayumba Nyamwasa, waulura kuti Paul Kagame akuba miyala ku DRC.
Zonsezi tafotokoza mu video ya lero. Page is not hacked & it will never be.

Tipereke chenjezo motere! Anyone who don't want to be attacked asiye kupanga sponsor anthu kuti azipanga attack anzake. This is as simple as ABCD.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

03 Feb, 16:40


Former Army Chief ku Rwanda waulura kuti Paul Kagame amaba miyala ku DRC

Bakili Muluzi Tv

03 Feb, 11:54


Pamene M23 ikulowera ku Southern Kivu mu mzinda wa Bukavu, pali chiopsezo cha nkhondo pakati pa Burundi ndi Rwanda.

Kodi Kagame akufuna chani? Zonse mu video yathu ya lero.

Bakili Muluzi Tv

03 Feb, 05:55


CEASEFIRE.

Koma mukamapitiliza sikuti tikusiyani. We will break the Ceasefire and start again.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

02 Feb, 20:29


Atsogoleri onse a UTM amachokera kwa Mutharika.
Chilima atayambitsa chipani chake, UTM imanyoza nkumati ku DPP kuli madeya okhaokha. Lero tawaonani zimene apanga. Olo Kabambe atachoka lero, UTM idzatengabe mtsogoleri wa DPP chifukwa ku team kwawoko kuli madeya okhaokha.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

02 Feb, 18:04


Bakili Muluzi TV has never liked Chilima manifesto even when he was alive. Ndie tikudabwa ena akufuna timukonde atamwalira. We are not cowards like Dalitso Kabambe amene analephera kulowa UTM Chilima alipo, koma nkukagula chipani pogwiritsa ntchito ndalama za Mulli mwini wake atatsikira ku masano.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

30 Jan, 07:10


Kwa nthawi yaitali takhala tikunena pano kuti, Paul Kagame amatumiza asilikali mmayiko a SADC kumapanga ukazitape. Robert Mugabe anawathamangitsa ku Zimbabwe pa nkhani yomweyi. Lero asilikali a Rwanda akupezeka ku Mozambique, Zambia ndi Malawi. Amanamizira mabizinesi ogula mbeu ndi kugulitsa mowa, koma zoona zake ndi ma agent a Kagame; amalandira salary mwezi ulionse ngati ma intelligence officer. Kuti muwafufuze ambiriwa ndi asilikali mdziko la kwawo.

Kamajekete wakhala akuthamangitsa ma refugee a ku Dzaleka ndi kumagwirizana ndi ma agent a Kagame. Lero asilikali a Malawi akuphedwa ku DRC chifukwa Kagame akudziwa zinsinsi zambiri za dziko lathu pogwiritsa ntchito ma agent amenewa. It's high time mayiko a SADC aunikenso ubale ndi Rwanda.
America simasekelera Russia kapena China agents mdziko lawo. Ngakhale Putin, akaona secret CIA agent ku Moscow amamutsekera kundende.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

30 Jan, 04:51


Kagame wayamba kuvomereza kuti asilikali aja anaphadi.

Ramaphosa anachenjeza Rwanda kuti akapitiliza kupha asilikali a SADC, that will be a declaration of war.

Ndie usiku wathawu Kagame wayankha kuti sakuopa dziko lililonse ku SADC including South Africa. Ngati akufuna nkhondo iyeyo ndi okonzeka kutero.
Wapitilizanso kunena kuti, asilikali a Malawi, Tanzania ndi South Africa akulimbana ndi Rwanda ku DRC ndipo nchifukwa chake akuphedwa. Paul Kagame wakananso South Africa kukhala peace mediator pa nkhondo imeneyi ndipo wamuuza Ramaphosa kuti;
"If you want confrontation, Rwanda will respond accordingly."

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

29 Jan, 17:51


Paul Kagame wapha asilikali atatu a dziko la Malawi ku DRC

Bakili Muluzi Tv

29 Jan, 14:20


President wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera lero walamula kuti otsatira chipani cha MCP asamapezekenso mma Airport pamene iyeyo akuyenda.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

29 Jan, 10:07


Breaking News!

Atamva kulira kwa anthu a ku Africa, Donald Trump wabweza ganizo lake losiya kuthandiza pa nkhani za umoyo. Iyeyu walengeza lero kuti chithandizo cha ma ARV, Zakudya komanso mankhwala mzipatala zipitilire.
Apatu onse amene amalandira ma ARV adyera nyama lero.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

29 Jan, 07:28


Director of Intelligence wa ku Nigeria akhala akufika mdziko muno mwachinsinsi. Atera pa Kamuzu International airport cha ku masanaku.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

28 Jan, 17:36


Police ikufuna kumanga Norman Chisale pa nkhani ya Certificate ya mizimu.

Bakili Muluzi Tv

27 Jan, 20:28


America yasiya kuthandiza ma ARV.
Amalawi agwire mtengo wanji

Bakili Muluzi Tv

27 Jan, 18:19


America yayimitsa chithandizo cha ma ARV ku Africa kuphatikiza Malawi kwa masiku 90. Lero tibwera ndi video pa nkhani imeneyi koma mochedwerapo.

Bakili Muluzi Tv

27 Jan, 15:34


Bakili Muluzi anachoka ku tambala wakuda kukapanga yellow. Bingu wa Mutharika anachoka ku yellow kukapanga blue. Joyce Banda anachoka ku blue kukapanga Orange. Chilima anachokanso ku Blue kukapanga Red.

Ndie tikudabwa ndi amthirakuwiri a ku Mulanje central. Wina anachoka ku Blue ndi kukapanga blue. Poyamba, colour ya odya zake alibe mlandu inali green. Lero asintha kukhala Red pofuna kusokoneza UTM.

Bakili Muluzi Tv

26 Jan, 16:07


Aphungu ena ku America akufuna Donald Trump ayimenso katatu.

Bakili Muluzi Tv

26 Jan, 08:02


NKHANIYI TIYIMALIZE MOTERE.

3 years before his birth, abambo ake akunenawo anali atasamuka ku Nyasaland kuno; amakhalira ku Tanganyika. Anabwelera ku Malawi around 1967. Pa nthawiyo iyeyu anali wamkulu kale & he don't claim anything about father and son relationship. Madalawo anafika kulowa mmanda ndipo sitinamve akuwakumba chibale.

Fast forward, tibwere nthawi yomwe Bingu anayambitsa chipani cha UP. Iyeyu anagulidwa ndi UDF ndi kupita pa Mjamba kukanyoza & this was the first time anabwera poyera kudzakumba chibale. Anthu a ku Thyolo atamva speech yake anamukana kuti si m'bale wao.
2019 anatulukiranso pa msonkhano wa UTM; 2023 anakumana ndi Nankhumwa wa PDP; Panonso wakaonekera pa msonkhano wa MCP.

Kodi chibale cha mtundu wanji chokumbana nthawi ya campaign yokhayokha?
Abambo ake akunenawo ali ndi ana awiri ndipo adakali ndi moyo; that is blood relative ngati akunenadi zoona. Sitinamve akuwatchula mmisonkhano koma akulimbana ndi munthu oti si m'bale wake.
NSANJE NDI UFITI.
HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

26 Jan, 07:19


Asilikali a Malawi akuphedwa ku DRC ndi asilikali a Rwanda. Monga tikuonera pachithunzipo, chigawenga cha M23 komanso yemweyo ndi msilikali wa Rwanda.

Tisanamizire zigawenga komano straight to the point; Paul Kagame ndi amene akupha asilikali a Malawi ku DRC. Tikuyenera kusintha dzina la msewu ku Lilongwe; kusakhale Paul Kagame Road ku Malawi.

Bakili Muluzi Tv

25 Jan, 23:12


DRC yathamangitsa ambassador wa Rwanda mdziko lawo. Izi zikutsatira kuphedwa kwa military governor, asilikali atatu a Malawi, 9 a South Africa ndi anthu ena ambiri masiku apitawa.

Rwanda ikupereka ndalama, malo ogona ndi zida za nkhondo kwa zigawenga za M23 ndi cholinga azichitira chiwembu asilikali a SADC ku dera la Kivu. Zimenezi zakwiyitsa president Felix Tshitsekedi yemwe walamula kuti ambassador wa Paul Kagame achokeretu ku Kishansa before 48 hours.

Bakili Muluzi Tv

25 Jan, 21:28


Dzina la player ameneyu ndi Frank Mussa & was also a Soldier. R.I.P

Bakili Muluzi Tv

25 Jan, 21:25


Player wa Red Lions waphedwa ku DRC ndi zigawenga za M23

Bakili Muluzi Tv

25 Jan, 17:25


Mabungwe a ku America anayambitsa bwanji nkhondo ya ku Ukraine

Bakili Muluzi Tv

25 Jan, 05:13


Masitima ndi ndege amadalira GPS akamayenda. GPS imagwirizana ndi malo otchedwa North pole amene amapezeka ku Arctic Ocean. Ngakhale nthawi imayambira kumeneko chifukwa ma Line a Longitude amene amapanga Time zone anadutsa komweko.

Panopa a science adabwa kupeza kuti North pole yasuntha. Poyamba malowa amapezeka mbali ya Canada, kenaka anasunthira ku Russia; masiku apitawa asuntha kwambiri kulowera ku Siberia.

Zimenezi zapangitsa kuti map asokonekere ndipo GPS yapangidwanso upgrade.

Masitima, ndege komanso galimoto zimene zimagwiritsa ntchito GPS poyenda, zimapanga track magnetic field ya North pole. Kusintha komwe kwachitika kwasokoneza kwambiri map amenewa.

North pole ndi malo odabwitsa kwambiri. Kulibe nthawi yokhazikika ngati kwathu kuno.Kuyenda kwa dziko kwapangitsa kuti nthaka isunthe ndi kusintha position ya malowa.

Bakili Muluzi Tv

25 Jan, 04:38


Dziwani kuti chi machine cha MACRA sichingagwire Bakili Muluzi tv. Kuulura zinsinsi za boma tinayambira kale koma opposition ikugona. Bakili Muluzi tv sidzayima nawo pa chisankho. Auzeni achina Atupele Muluzi ndi andale anzawo azikulankhulirani. Ifeyo tizilankhula za ndale tikafuna but our concentration now ikhala pa History.

Bakili Muluzi Tv

22 Jan, 13:40


Saulos Chilima asanamwalire, Bakili Muluzi tv imamudzudzula ndipo iyeyo amamvera ndithu; Mwina enanu mukutitsatira kumene koma dziwani kuti Ife sitinyengelera wandale aliyense akalakwitsa.

Onse amene anathawa DPP atatola chikwama nkumanamiza anthu kuti angasinthe zinthu, tithana nawo.

Bakili Muluzi Tv

22 Jan, 08:37


Bakili Muluzi amanyoza MCP chikhalirecho anali nduna komanso Secretary general ku MCP komweko.

We will not tolerate people to insult DPP chikhalirecho amadyelera komweko. Ngati Nankhumwa ndi Kabambe akunena kuti DPP is a problem ndie kuti nawonso ndi vuto lalikulu.
Sitilora kuti wina wake anamize amalawi ngati muja zidachitikira 2020.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

22 Jan, 08:20


Akuti anthu omuzungulira APM amamusokoneza.
Amenewa ndi mawu ochokera ku zipani zina.

Kodi Dalitso Kabambe sanali mmodzi omuzungulira APM? Chuma chonse akugawa ku UTM anachitenga kutiko? I hope he was Reserve Bank Governor mnthawi ya a Mutharika.

Grezedar Jeffrey, Uladi Mussa komanso Brown Mpinganjira; anali ma advisor a Mutharika. Lero ali ku MCP kunamiza anthu kuti APM anali oyipa. Afunseni kuti chuma chonse chija anachipeza bwanji.

If APM inner circle was bad, siyani kutamanda Dalitso Kabambe chifukwa anasulidwa ndi Mutharika yemweyo. Zoipa mukumutulira Chisale ndi Mukhito, zikakhala zabwino mukupatsa amene alowa zipani zanu. Kukhala satero ai.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

21 Jan, 16:45


Matenda a Jose Chameleon wa ku Uganda

Bakili Muluzi Tv

21 Jan, 06:52


Pastor Martin Thom anali mlangizi wa President. Pakhomo pake ndi pa mwana alirenji. Ndi mmodzi wa ana a bambo Karan Thom Mutharika. Ndi chifukwa chani akulu amenewa sakupempha mwana wao koma busy kuyipitsa mbiri ya munthu osalakwa?

Ngakhale pa interview imene anapanga ndi MBC, sanatchule za ana ndi zidzukulu zawo zimene zikuchita bwino mntaunimu. Nkhani amangokhalira Bingu ndi Peter. Kodi ufiti ungapose apa?

Bakili Muluzi Tv

20 Jan, 20:12


Chithunzi cha lero tikuona nduna ya za ulimi; nduna ya maphunziro komanso Vice President.

Onsewa anachoka ku Lilongwe ndi entourage yawo ulendo ku Dowa kogawa phala pa sukulu ya primary.

Bakili Muluzi Tv

20 Jan, 16:42


China ndi America kulimbirana mgodi wa Tiktok.

Bakili Muluzi Tv

20 Jan, 14:44


Meeting ya ku Area 30 police headquarters amanga mfundo zingapo.

1. Mfuti za ku Israel zigawidwe kwa anyamata a zikwanje pasanathe 2 weeks from now.

2. Ackis Muwanga anafunsa Director of CID kuti ndi chifukwa chani analephera kumanga Norman Chisale pa ShopRite ya ku Blantyre.The task has to be done as soon as possible.
Komabe CID Director anamukanira ponena kuti last time anamupusitsa pamene anapita kukamanga Chisale without Arrest warrant.
Potero, Ackis Muwanga wamutsimikizira CID Director kuti ayesetsa kukambirana ndi magistrate kuti apeze Arrest warrant posachedwa,ndipo Chisale asatulukenso kundende up to October 2025.

Ma report otsimikizika atiuza kuti after Chisale arrest, Ackis Muwanga akukonza plan yothana ndi Peter Mutharika pogwiritsa ntchito zigawenga. Panopa apolisi ena ndi okwiya atamva kuti mfuti zoopsa za ku Israel zikupita kwa anyamata a zikwanje.

Tikupatsirani zambiri zikamachitika.

Bakili Muluzi Tv

20 Jan, 10:23


Ku Ndirande amadziwika ngati mbava komanso kabwerebwere wa ku polisi. Ku Chiradzulu mukampeza mammawa omwe waledzera kachasu; Ngati alibe yomwera amapezeka pa bawo. Amatchuka ndi ufiti pa mbumba pawopo.

Chibadwire pa moyo wake sanakumanepo ndi Prof Peter Mutharika. Akunama kuti amalumikizana ndi Bingu mpaka anayambitsa nawo chipani popanga logo ya Chimanga 4. Nanga nchifukwa chani ali munthu osauka mpaka lero? Why blaming APM za umphawi wake chikhalirecho anali ndi mwayi othandizidwa ndi Bingu?

Akuti amacheza ndi ana a Bingu; Then bwanji sanawauze omwewo kuti amuthandize? In addition, APM ndi Bingu ali ndi zidzukulu zambirimbiri zochita bwino; ena ali ku Europe and America. Bwanji sakumuthandiza if he is indeed a good man and brother wa Bingu? Magulu a Namondwe amapezeka ku Thyolo komweko; bwanji sakumuchita support?

The worst part of it, analumikizana ndi Kamajekete kukanyoza the so-called brother pa msonkhano. How can you be a good brother yet you are behaving like Judas Iscariot?

Bakili Muluzi Tv

19 Jan, 16:12


Mayiko a Swaziland ndi Lesotho, amapezeka mkati mwa South Africa chifukwa chani?

Bakili Muluzi Tv

19 Jan, 09:06


Ambiri tili ndi zibale za patali. Zibale zochokera kwa agogo awo a agogo athu komanso ena ochokera ku zisuweni za agogo athu. Ambiri akuyendera ma Prado, ifeyo njinga za kapalasa. This is normal ndipo zili common mmadera ambiri a dziko lino.

Chodabwitsa kwambiri, anthu amakokera zibale zotere akaona kuti munthuyo ndi olemera.
Kuti mufufuze akulu amenewa, ali ndi zidzukulu kwawo komweko zovutika; koma sangazikumbe chifukwa cha umphawi. Amakumba zibale za patali zimene zikuchita bwino kuti apeze mwayi wa chuma.

Bakili Muluzi Tv

19 Jan, 08:36


Munthu wa mtundu wanji omangolumikizana ndi adani a the so-called brothers? Poyamba anakumana ndi Nankhumwa atagalukira DPP; Pamene anali nduna ya Peter sitinamuone akupita kukakumana ndi akuluwa. Atamuchotsa mchipani cha DPP, anathamangira ku Chiradzulu kukakumana ndi the so-called Mutharika.

Lero walandira ya mchere kwa Kamajekete. Paliponse pamene akulankhula za ubale umenewu, akupopedwa ndi adani a Mutharika.

Kwawo ku Chiradzulu amatchuka ndi mbiri za ufiti. Mutharika Brothers anali anyamata a sukulu. Iyeyu chinavuta ndi chani osaphunzira?

Bakili Muluzi Tv

19 Jan, 08:19


Mbiri ya akulu awa, akuti Karan Thom Mutharika, tili nayo. Tsiku lina tikatopa tidzayiphulitsa.

Ngati akunena zoona kuti Peter Mutharika ndi m'bale wao, ndi chifukwa chani Bingu sanawathandize mu zaka 7 za ulamuliro wake? Akutanthauza kuti Bingu ndi Peter onsewo angakhale akhungu osazindikira kuti uyuyu ndi brother wao?

Kumudzi kwawo amatchuka ndi mbiri za ufiti koma tikadzafotokoza zonse, Jezebel adzatumiza police komanso Daudi Suileman adzaonjezera budget ya Bakili Muluzi TV kufika pa 10 billion kwacha.

Bakili Muluzi Tv

18 Jan, 21:40


Bwana wa Tiktok, Mr Shou Zi Chew, akakhala nawo pa mwambo olumbilitsa Donald Trump. Izi zikudza pamene kampani yake yapangidwa ban ku America.

Poyambilira anampatsa ma condition; agulitse kampani kwa munthu wadziko lina chifukwa ma China akumagwiritsa ntchito pochita ukazitape ku America. Atakana kutero, Joe Biden wachita ban Tiktok; App yawo ikuyenera kuchotsedwa pa Google ndi Apple store kuyambira mawa. Ngati Google inyozere chigamulo chimenechi posachotsa Tiktok app ku play store, adzalandila chilango kapena kupereka chindapusa cha ma billion ankhaninkhani ku boma.

Komabe mwayi udakalipo; president wa tsopano, Donald Trump, akhoza kubwera ndi chilango china kupatula Ban. Let us wait and see.

Bakili Muluzi Tv

17 Jan, 18:49


Mitembo ya anyani inapezeka bwanji kumwamba?

Bakili Muluzi Tv

17 Jan, 11:32


Timuyamikire potseka kampani yosatsata malamulo. Koma tikutsutsana naye chifukwa alibe communication skills. Malamulo onse ali mmanja mwake as a Minister; akhoza kulamula police kunjata ngati mmene wachitira ndi mwini kampani. Chopangira harass mzimayi nkukhala chiyani?

Bakili Muluzi Tv

17 Jan, 11:23


Kupatula kugwira pambali pa bele, andunawa amaloza chala komanso kulankhula mokalipa. Tithokoze kuti anakumana ndi mzimayi odekha; otherwise akanakhala munthu wa phuma ngati mmene akuchitira iwowa, police ikanalowelerapo.

Not all people can accept to be insulted that way. We must learn communication skills.

Bakili Muluzi Tv

17 Jan, 11:11


Ena akuti andunawo sanalakwitse kumugwira mzimayi uja. Tingoyerekeza mzimayi nayenso anabwezera kuwakwenya a minister malaya; zikanakhala bwanji?

Paliponse ulemu ndi ofunikira. Nduna imakhala ndi omuthandizira komanso achitetezo. Zomwe anachita kumugwira mzimayi uja si ntchito yake. In short, that is harassment of women. Munthu akalakwa samanena kuti mumuchite chipongwe. Pali malamulo amene amayenera kutsatidwa.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

17 Jan, 10:04


Vitumbiko Mumba akugwira ntchito yake ngati nduna koma walakwitsa kumugwira mzimayi molakwika; that is harassment ndipo malamulo agwire ntchito. Dziwani kuti unnecessary physical contact including unwanted touching on women is harassment. Akanakhala otsutsa boma police itammanga kale komanso CHEFO ikanatulutsa statement.

As far as we recommend Mr Mumba potseka kampani, temper yawo yawalakwitsa pogwira mzimayi popanda chilolezo;That is Harassment.
Abusa a ku Zolozolo anawatsegulira defamation case ngakhale amanena zoona. Ndie apa zisakomere mbuzi kugunda galu.

Bakili Muluzi Tv

17 Jan, 09:40


Mkazi wa mwini samagwilidwa choncho. Anduna chepetsani ma temper. Akanakhala mayiko ena mlandu unakwanira apa.

Bakili Muluzi Tv

17 Jan, 08:55


Anthony Bendulo anasokoneza nawo passport system. Anamulonjeza kuti akabuloka system, akhala nawo mu team yopindula ndi contract ya tsopano. He was part of the crew yoononga passport system ku Chilambula data center.

Zimene akulankhula lero ndi mphamvu yokhumudwa chifukwa sanapindule mu new contract. In addition, anamuchotsa ngati ICT Director ku OPC. Pokwiya, iyeyu anatenga Prado kukayisiya pa BICC. A Boma anakayitengera pomwepo ndipo ntchito yake inatha.

Mmbuyomu pamene timakamba kuti passport system yaonongedwa mwadala, Anthony Bendulo anali mmodzi wa anyamata a MCP amene amatsutsana nafe. They were saying we are doing propaganda. Lero wayamba kuulura chifukwa wachotsedwa ntchito ndi Colleen Zamba.

HISTORY IS THE BEST TEACHER.

Bakili Muluzi Tv

17 Jan, 07:34


Abel Muyabah; Nkhani yake tinakamba kale.

Anali bodyguard wa Chimwendo Banda.
Anaba 200 million ya Boma.
Amagwira ntchito ku State House.
Ndi mmodzi wa anyamata a zikwanje.
Anali mu gulu lokhapa anthu ku Mbowe.
Anavula azimayi a DPP pa Manda a Kamuzu.
Panopa ndi bodyguard wa Baba Malondera.
Dzulo anali nawo mu gulu la anyamata a ku Lilongwe amene anaperekeza nduna za boma ku Ndirande.

Bakili Muluzi Tv

16 Jan, 17:27


Akuluna ayamba kuphedwa ku DRC;
Donald Trump akufuna kugula chilumba cha Greenland.

Bakili Muluzi Tv

15 Jan, 20:08


Azimayi anavulidwa zovala za mkati pa Manda a Kamuzu ndi anyamata a MCP. Mwina a CHEFO ayiwala.

Mu ndege ya ku Chikangawa munalinso azimayi awiri.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

15 Jan, 19:42


Azimayi a DPP atavulidwa ku Mponela, CHEFO inakhala chete.
Mzimayi wa DPP ataomberedwa ndi apolisi dzana, CHEFO inakhala chete.
Azimayi a MCP atakuwidwa ku Ndirande, CHEFO yatulutsa statement ndi kulankhulapo.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

15 Jan, 18:33


Ku mwambo wa John Chilembwe, anyamata a MCP acheka Mr Geoffrey Kukada a chipani cha UTM.

Izizi Jezebel sangafufuze mpang'ono pomwe koma akanakhala wa chipani chotsutsa, kalekale atammanga.

Bakili Muluzi Tv

15 Jan, 15:15


Atakhutitsa mimba zawo nkuyamba kugeya, ayambapo kudandaula kuti chakudya chikuwawa.
Passport saga, ASYCUDA System kupangidwa delete ku MRA; Kamajekete kutulutsa ma passport a fake; zimachitika mnthawi yomwe Anthony Bendulo anali ICT Director ku office of president and cabinet.
Lero wayambana ndi Colleen Zamba, msuzi wauma; wayamba kuulura. Kodi anali kuti zaka zonsezi?

Allan Ntata anali Lawyer wa president Bingu. 2012, just few hours atamwalira, anatuluka DPP kukalowa PP ya mayi Joyce Banda.

2014 APM atabwelera m'boma, Ntata anayesera njira zosiyanasiyana kuti abwelere ku State House, zinamukanika. Potero anayamba kulimbana ndi onse amene anamuyandikira Mutharika. He thought they were the ones blocking him; the likes of Peter Mukhito and Norman Chisale.

Kumbukirani kuti Bingu atamwalira, Allan Ntata anaba ndalama ndi kuthawira kwa mayi Joyce Banda. Ngati brother wa malemu, Peter anali okwiya ndi khalidwe losakhulupilika la mnyamata ameneyu; hence the blocking in 2014.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

15 Jan, 07:17


George Kasakula analephera ma interview ku MBC; Amene anachita bwino ndi Dr Jolly Ntaba. U Director General anaupeza mothandizidwa ndi Richard Chimwendo Banda.

Ngati mukukumbukira bwinobwino,Zilani Khonje anali Director of news and programs ku MBC. Board inamuchotsa ntchito chifukwa samagwirizana ndi George Kasakula.
Panali tsiku lina, Flora Suya anapita ku maofesi a MBC pa Chichiri; anauza alonda kuti akufuna kukapanga filimu mu ofesi ya amuna ake bambo Kasakula. Ma guard anali odabwa chifukwa zimenezi zinali zachilendo; anathamangira kwa Zilani Khonje kukamudziwitsa. Ngati director of programs,anamuletsa mkaziyu kulowa mu ofesi. Flora anamuyimbira mamuna wake yemwe anayamba kumukalipira Zilani Khonje. Anamulora mkazi wake kuka-shooter video mu ofesi zomwe ndi zoletsedwa pa malamulo a MBC. After the incident, sipanatenge miyezi, Zilani Khonje contract was never renewed by board of Directors.

In addition, malamulo amaletsa MBC Director general kulankhulapo nkhani za ndale.

Bakili Muluzi Tv

14 Jan, 20:14


Tioneko zimene SOSISA yatikonzera mchaka cha 2025.

Potengera chipepala cha ku treasury chimene tapeza, abwereka 133 billion kwacha mmwezi uno wa January. Mafuta a galimoto atenga pa ngongole ndi kupinyolitsa fodya wa alimi.

February ayika plan yobwereka 112 billion; March 153 billion. Ndie akuchotsa ndalama ya ngongole yomweyo kukagulira chi machine cholimbana ndi Bakili Muluzi tv.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

14 Jan, 19:18


Asilikali anaukira Boma la Kenneth Kaunda kawiri konse. Chinavuta ndi chani

Bakili Muluzi Tv

10 Jan, 18:42


Ku Malawi kukuchitika zinthu.

Mabanki apeza kuti anthu ena akubweretsa ma ID a fake podzatsegula ma account. Izi zikuchitika patangotha masiku ochepa aphungu atagwira NRB yakuba ku NFRA Kanengo warehouse.

Ku ma boarder ena akubwezedwa ndi ma passport opangidwa ndi Nick Chakwera. Nayonso system ya Smartmatic yasokonekera. Ikakhala nkhani yosowa kwa mafuta, police brutality and corruption;it's part of life.

Ku Senegal, anyamata awiri anamangidwa ndi apolisi 2023. Ousmane Sonko akuti amayambitsa zipolowe; Bassirou Faye amasakidwa ngati muja MCP imachitira ndi Bakili Muluzi tv. Atamugwira,anamutsekera kundende miyezi 9. Koma ndikunena pano, awiriwa ndi atsogoleri a dziko la Senegal. Faye ndi President ndipo Sonko ndi Prime minister.
Kumangidwa kwawo kunaonjezera mavoti ndi kugwetsa boma lolamula mmwezi wa April 2024.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

10 Jan, 17:33


Lazarus Chakwera walamula polisi ndi makhothi kuti achite chotheka pomanga akuluakulu 17 a Opposition tisanayambe campaign. Mayina awo ali motere;

1. Norman Chisale
2. Shadreck Namalomba
3. Dalitso Kabambe
4. Alfred Gangata
5. Peter Mukhito
6. Sameer Suileman
7. Charles Mchacha
8. Joseph Mwanamveka
9. Lloyd Muhara
10. Mary Navitcha
11. Enock Chihana
12. Timothy Mtambo
13. Jappie Mhango

Komanso pali anthu 4, ma former CEO and Directors a makampani a boma.

Funso nkumati, zaka 5 zonsezi anali kuti osawamanga? Alfred Gangata ndi Norman Chisale ali pa top list yosakidwa ku Malawi Congress Party. Meeting ya dzulo usiku ku Area 47, Chimwendo Banda wauza mnyamata wa mkono umodzi; aonetsetse kuti Chisale akaseve jele tisanayambe campaign.

Bakili Muluzi Tv

10 Jan, 11:32


Good afternoon

HISTORY IS THE BEST TEACHER.

Bakili Muluzi Tv

09 Jan, 18:30


President odziwa kuongola mafupa komanso kuphulitsa zithupsa.

Bakili Muluzi Tv

09 Jan, 16:29


Anatiuza kuti ndege inagwera kowilira asilikali sangafikeko.
Posachedwa anyamata a zikwanje amavuta ku Lilongwe sanalankhule chilichonse; Kwa Nsundwe ena anatseka mnsewu dzuwa likuswa mtengo; Ngakhale Blackbox mu ndege ya Chilima is still a mystery.

Poti ayamba okha kuyankha za ndale, tikukhulupilira atiuza kumene Chakwera anabisa Blackbox.

Sitifooka! Sititopa! Sitiopa!

Bakili Muluzi Tv

09 Jan, 15:15


Ngati mdziko muno mulowe ziwawa, oyambitsa wake akhala Jezebel. Boma linapha Chilima ndi kubisa Blackbox; Lero ukawafunsa samayankha chilichonse. Kutiona kupusa? Kapena mukuyesa tingayiwale imfa ya nkhanza kwa abale athu okwana 9 ku Chikangawa? Ifetu timaona ngati kalata imene mukutulutsa mutiuza nkhani ya Blackbox.

Police ikuteteza anyamata a zikwanje. Posachedwa anatiuza kuti agwira angapo koma sitinaone akupita ku khothi, even mayina awo sanatulutse. Akuwateteza bwanji poti anthuwo ndi zigawenga?

Jezebel akamakhala azidziwa kuti majority malawians yatopa ndi polisi ya MCP. Akapitiliza nyasi zakezi dziko aliyatsa moto.
Malawi si Rwanda ndipo wina asamadzinamize kuti angalande democracy imene agogo athu Chakufwa Chihana adavutikira 1992.

Bakili Muluzi Tv

09 Jan, 13:39


Lero Lachinayi nthawi ina iliyonse, boma la Malawi litulutsa chikalata chimene chichenjeze mzika za dziko lino kuti aliyense otseka mseu popanda chilolezo adzazengedwa mulandu.

Izi zikutsatira misonkhano yoimaima imene mtsogoleri wakale wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika anachititsa lachitatu mu mzinda wa Blantyre kumene zikwizikwi za anthu zinafika kudzamuchita sapoti komanso kuonetsa mkwiyo ndi boma lankhanza la Malawi Congress Party.

Zikuoneka kuti apanikizika ndipo abalalika.

Bakili Muluzi Tv

09 Jan, 07:27


Anadziwa bwanji kuti adzalamulira 10 years poti kunali mgwirizano ogawana ma telemu ndi Chilima?

Apapa mfiti imene idagwetsa ndege ku Chikangawa yadziulura yokha.

Bakili Muluzi Tv

08 Jan, 22:36


Mutharika anatseka mzinda wa Blantyre

Bakili Muluzi Tv

08 Jan, 19:18


Chakwera akufunika ku mental hospital akamuyeze ubongo

Bakili Muluzi Tv

08 Jan, 08:55


Good morning

Lazarus Chakwera akufuna zaka zina 5. Wayiwala kale zimene anatiuza 2020👇

"If I don't change everything in 2 years, I will resign."

Zambiri mu video imeneyi.

Bakili Muluzi Tv

08 Jan, 05:40


Atasankhidwa kukhala full minister, Chomanika anaitana mafumu a ndodo ku Lowershire kukawathokoza chifukwa chokapempha Chakwera ku Chikoko Bay kuti amuike kukhala full Minister. Kenaka anauza mafumuwo akonze mwambo okamudzodza kukhala Mbuya wa Shire Valley kulowa mmalo mwa Gwanda Chakuamba. Anapitilira kuwauza mafumuwo kuti Mbuya sangakhale Mkaladi, choncho kuchoka Gwanda, palibepo walowa mmalomwache.

Mafumu ataimva nkhaniyi, sanamuyankhe koma kumbali akambirana kuti Chomanika ndi khombwani ndipo sangakhale Mbuya wa ku Shire Valley.

Chomanika yemwe wakhala akupereka ma 5 000 kwa ma membala a DPP ponena kuti iye sanatuluke chipani, ngwadyera chifukwa ndi nduna ya Chakwera, amapezeka mmisonkhano ya MCP nkumanena kuti boma ndi lomweli; Akapita kwawo ku Chikwawa akuuza masapota ake kuti adzayima independent pa 16 September.

Bakili Muluzi Tv

07 Jan, 19:10


Dr Bakili Muluzi anasiya inflation ya 15%. Bingu anayitsitsa kufika pa 6%.

2014, Joyce Banda anasiya inflation 35%. Peter Mutharika anayitsitsa kufika pa 8%.

Chakwera anapeza inflation ya 8%. Pano wayikweza kufika 35%. Ndie kaya mafupa amene akuongolawo ndi ati, mwina a ku Chikangawa kapena.

Peter Mutharika anamusiyira Forex ya 1 billion dollars; Lero alibe chilichonse angoyendera hand to mouth. Kodi zithupsa zomwe akuphulitsanso ndie ziti?

Akuluakulu! Utsogoleri ndi mphatso yochokera kwa mulungu, sakakamiza ai. Munthu walephera 5 years nkumapempha anthu kuti akuvoterenso ndie uchitsiruwo.

Dr Bakili Muluzi analonjeza nsapato sanakwaniritse, koma at least zinthu zina ngati sukulu yaulere, ufulu olankhula, kuthetsa makhadi, ufulu wa bizinesi, mijigo, zipatala zaulere anakwaniritsa. Inuyo a Chakwera pa zomwe munalonjeza 2020, ndi chani chimene mwakwaniritsa? Ngakhale ufulu olankhula umene mwatilanda.

Mnzanu anakuyikani pa mpando, mapeto ake kumupha, blackbox kubisa; Kodi ufiti ungapose pamenepa?

Bakili Muluzi Tv

07 Jan, 18:00


Malipoti amene tapeza ku Area 30 akunena kuti, m'bale wake wa Chakwera, Ackis Muwanga, wayitanitsa commissioner Noel Kayira ku police headquarters kuti akamukalipire chifukwa cholephera kuombera masapota a DPP. Panopa communication kuchokera kwa Jezebel yafika kale ndipo commissioner Dr Noel Kayira PHD, akukonzekera ulendo wa ku Lilongwe.

Tipemphere abwereko ndi thanzi chifukwa MCP imadana ndi apolisi a chitumbuka. Sweetman Kumwenda anamuphera ku Mikuyu Prison ndipo mtembo wake anausowetsa.

HISTORY IS THE BEST TEACHER

Bakili Muluzi Tv

07 Jan, 16:46


COMMISSIONER NOEL KAIRA ASAMUSIDWA CHIFUKWA CHOKANA KUPHA MA SUPPORTER A DPP

Mmodzi mwa ma Commissioner ophunzira bwino kwambiri a Police m’dziko muno Bambo Mlowoka Noel Kaira wasamusidwa mwankhanza kuchoka ku Blantyre kupita ku Lunchenza, m’boma la Thyolo.

A Kaira PhD, anali Commissioner wa Police ku chigawo chakummwera ndipo akudzudzulidwa ndi boma la MCP chifukwa sanalamule a Police kuti aponye teagas komanso kuombera zipolopolo kwa ma supporters a DPP amene anachezera kuimba panja pa Blantyre Police Station podikilira a Sameer Suleman kuti atuluke mu ndende.

Usiku wa Lolemba, Jezebel analamula Commissioner Kaira kuti athamangitse anthuwa ndi tear gas komanso zipolopolo koma a Kaira anakana kuti ntchito ya Police sikukhetsa mwazi wa anthu.

Chodabwitsa kwambiri ndi chakuti a Noel Kaira anabweretsedwa ku Blantyre kudzalowa mmalo mwa Commissioner Richard Luhanga amene anaponyedwa ku Mzuzu.

Bakili Muluzi Tv

07 Jan, 15:12


Breaking News!

Nkhumba Chimwendo Banda walamula apolisi achotse ntchito commissioner Noel Kayira amene amayang'anira chigawo cha kummwera. Ndikunena pano Jezebel wapanga transfer Noel Kayira ku Luchenza m'boma la Thyolo. Akuti analakwitsa kumpititsa Sameer Suileman ku khothi; amayenera kumusunga kaye mu cell kwa one week.

Panopa nkhumba Chimwendo Banda walamula Jezebel kuti atumize commissioner Emmanuel Soko kukayang'anira southern region. Iyeyu ndi membala wa MCP.

Tikupatsirani zambiri zikamachitika

Bakili Muluzi Tv

07 Jan, 09:31


Hon. Sameer Suileman kulankhula atatuluka kundende.